MISALA/MPATUKO M’MAGANIZO — (en. Schizophrenia)

Misala/Mpatuko M’maganizo ndi chiyani?

Matenda amene amakhudza mmene munthu amaganizira, kukhudzidwa ndi khalidwe lake.

Chimene chimayambitsa matendawa sichidziwika kwenikweni, koma zinthu izi pamodzi, kutengera/kuyamwira, zochitika pamalo amene munthu amakhala, kusintha kwa magwiridwe ntchito kwa bongo ndikukhala Mwale zimachititsa kuti munthu adwale matendawa.

Anthu amene ali ndi matendawa amaonetsa maganizo oti munthuyu ali mudziko layekha, amakhala ndi malankhulidwe ndi makhalidwe nosokonekera, ndiponso amakhala osachita zinthu ndi anthu ena. Muvuto okhala ndi maganizidwe opelewera ndi kuyiwalayiwala amatha kukhalaponso.

Thandizo limakhala la moyo wonse, ndipo limakhala losiyanasiyana monga mankhwala, kuyankhulitsana ndi adokotala.

Anthu ambiri amene ali ndi matendawa samachita ziwawa kwa anthu ena ndipo sapereka chiopsyezo kwa anthu ena.

Zizindikiro za Matendawa akamayamba

Zizindikiro za matendawa zimakhala azosiya kwa anthu osiyana. Nthawi zina zizindikiro zimayamba pang’onopang’ono kwa miyezi kapena zaka, nthawi zina mwadzidzidzi. Wodwala amatha kupeza bwino nthawi zina, patsogolo mkudza yambiranso.

Khalidwa limene limaonekera Matendawa akamayamba

 • Kumva kapena kuona zinthu zoti palibe
 • Kumaona ngati ngati anthu akukuyang’ana kapena kukulondora
 • Malawnkhulidwe achilendo ndipo osamveka
 • Makhalidwe athupi odwabwitsa
 • Kuchita zinthu mosemphana ndi m’mene malo alili
 • Kutsika kwa kakhonzedwe ka maphunziro kapena kagwiridwe ka ntchito
 • Kuchepa kwa kuzisamalira thupi ndi mavalidwe onyansa
 • Kusintha kwa khalidwe la munthu
 • Kusacheza ndi anthu ena
 • Kukhala okwiya nsanga kapena mantha ndi achibale
 • Kukanika kugona kapena kuika ganizo pa chinthu
 • Khalidwe losagwirizana ndi pamalo kapena khalidwe la chilendo kwambiri
 • Kukhala ndi maganizo kapena kukopeka ndi zipembedzo zachilendo

Zizindikiro za Matendawa

Zizindikiro zimene zimaonjezereka ku khalidwe la munthu — Positive symptoms

 • Maganizo kapena chikhulupiliro cha bodza — (Delusions). Munthu amatha kuganiza kuti anthu akumuyang’ana, kapena kuti iye ndi munthu wotchuka kwambiri (monga Yesu)
 • Kuona, kumva,  kununkhiza, kulawa zinthu zoti palibe — (Hallucinations). Nthawi zambiri zimakhala kumva mau akufotokozera zimene munthu akichita kapena kumamutuma zoti achite.
 • Maganizidwe ndi mayankhukidwe osokonezeka –(Disorganised speech) – kuyamhkhula zinthu zosamveka, kubwereza mau kapena maganizo amodzimodzi, kunena mau omveka chimodzomodzi koma osagwirizana.
 • Khalidwe kapena machitidwe osokonezeka — (Disorganised behaviour)– monga kulephera kusamba mthupi, kuvala zovala zosachapa, kukwiya mwadzidzi popanda chayambitsa chooneka, kusakhazikika, ndipo kuckita zinthu mosaziletsa.

Zizindikiro zimene zimachepa ku khalidwe la munthu — Negative symptoms 

 • Kusakhala ndi chidwi chokhala ndi anthu ena –(Social withdrawal)
 • Kusakhala ndi chilakolako kapena chidwi chochita zinthu — Extreme apathy (lack of interest or enthusiasm)
 • Kukhala opanda luntha pa zinthu — Lack of drive or initiative
 • Kusakhudzika ndi zinthu — Emotional flatness

Ngati muli ndi mavutowa kapena wachibale wanu, pezani madokotala adziwa mavutowa.

Author: chipikadzongwe

Psychiatrist